Friday, October 4, 2024
الرئيسيةLatestOOPS!MINISTERS' MG 2 ATTACK T/A NJEWA, VILLAGEMEN OVER LAND

OOPS!MINISTERS’ MG 2 ATTACK T/A NJEWA, VILLAGEMEN OVER LAND

KENYATTA: Granted the injunction

Mayi wina yemwe dzina lake ndi Isabel Tungande watukwana mafumu komanso watseka mseu omwe anthu a mmudzi mwa a Makalani  ndi Senza akhala akudutsa mmbuyo momsemu.

Mseu umenewu unalumikizitsa midzi iwiri, mudzi wa Makalani ndi Kasiyafumbi mpaka anthu amakafika ku Ntandire akadutsa nseu umenewu.

Koma ngakhale mafumu akuyesetsa kuti msewu umenewu usatsekedwe koma ukule chifukwa ndiofunikira kwambili, mayiyo watemetsa nkhangwa pa mwala  chifukwa amanyengana ndi nduna ina yomwe yangosakhidwa kumene.

Even A TA Njewa anapondapo nkunena kuti pali nseu ofunika koma mayiyu wanyoza mfumu yaikuluyo komanso mafumu onse omwe anabwera atatumidwa ndi a T/A kuti akalongosole za nsewuwo.

Mochita challenge, mayiwu wauza mafumuwo kuti iwowo alibe  mphamvu zomuuza zochita chifukwa malowo ndiake ndipo adagula yekha ndindalama zake.

Ndipo adapitiliza kuwapanga challenge a T/A Njewa kuti ngati akufuna kuyankhula naye galimoto ya amuna ake omwe ali a Minister ikawatenga abwere nawo kunyumba kwake.

Mafumu anyozedwa kuti ngakhale iwowo anagamula kuti pali nseu iyeyo nkhaniyo akupita nayo kukhoti chifukwa pali anthu ena omwe iyeyo akudana nawo kuti asamaduse nsewuwo. 

Pofufuza mafumu apeza kuti anthu omwe akudana nawo ndi ma neighbor ake.  Akuti asamadutse nseu wapakhomo pake. Zifukwa zake zodziwa yekha. Nkomwenkomwe nseuwo ndi wa public.

Pano poti achibwezi ake apatsidwa unduna wapeza mphamvu zambili zotseka nseu ndipo anthuwo asevedwa ndi ma pepala a injunction omwe ma date ake akuonetsa kuti analembedwa chaka cha 2021 Nthawi yonseyi amawasunga nthumba! 🤣

 A Justice Nyirenda ndiomwe asayinila chiletso chodutsa nsewuwo. 

A Officer Incharge a pa Chitedze Police Station nawonso analipo pamilandu yomwe mafumuwo adayitanitsa. Chifukwa adauzidwa kutelo ndi Anduna.

Funso lochoka kwa mafumu nkumati;  Kodi mphanvu zolamulira anthu kumudzi zayambano kuchoka kwa zinduna? Kodi tayambanso kuyenda chamfutambuyo!  Kodi democracy ija kani ndimeneyi.

Mafumu nawo pofuna kuonetsa mphamvu zawo adamuuza mayiyo kuti zisadzamuonekele adzapita kwa Maloya(Lawyer) kuti adzamuthandize. 😡

Nkhaniyi ikupitililabe ndipo mafumu nawo akutemetsa nkhwangwa pamwala kunena kuti milandu ikakhala pakati pa mayiyu Isabel Tung’ande Vs Chiefs & people of Makalani Village.

Zidze pano mzatonse nduna uku ziyaluka chifukwa chochengeta azimayi a mtseri. Ndunayo muyidziwa pompano mafumu akaloleza kuti tiyitchule dzina lake.  Koma akuti ndiya ku Nkhata Bay.

مقالات ذات صلة

ترك الرد

من فضلك ادخل تعليقك
من فضلك ادخل اسمك هنا

- Advertisment -
Google search engine

الأكثر شهرة

احدث التعليقات