Ulosi wa Prophet Rodrick Mtupa wakwanilitsidwa

0
162
Kanema yemwe wafala kwambiri pa masamba a mchezo a Facebook ndi Whatsapp akuonetsa, munthu wa Mulungu Prophet Rodrick Mtupa, akulotsera zomwe zachitika dzulo ku Limbe mu Mzinda wa Blantyre komwe apolisi komanso ogwira ntchito ku khonsolo ya mzinda wu anayendesedwa wa uyo! Uyo! ndi anthu okwiya.

Apolisi-wa anawona za malozazi pa nthawi yomwe anapita ku msika wa Limbe ndi cholinga chokagwira a malonda (Ma Vendor) omwe amachita malonda awo m’malo osayenera; komatu phuno salota, osaka-wa anasanduka wosakidwa pomwe ochita malonda okwiya wa anayamba kuwagenda mpaka kuthawa liwilo la mtondo wodowoka.

Koma malingana ndi Kanema amene anthu akugawana pa makina a internet, zomwe zachitika ku Limbe zinalotseredwa kale ndi Prophet Mtupa a utumiki wa Holy Palace Cathedral International, kutero kuti panalibe cha chilendo.

“Kuzakhala kuukira kwa anthu; ndipo m’maso anga auzimu ndikuwona gulu la anthu litagwirana manja ndi kumagenda anthu a boma(a polisi komanso ogwira ntchito ku city), izi zichitika ndithu,” anatero Prophet Mtupa mu Ulosi wawo wa kumayambiliro a chaka chino, akulotsera zomwe zachitika dzulo lachiwiri ku Limbe.

Pakadali pano, Mneneri wa apolisi ya Limbe Aubrey Singayamwa wati apolisi akhazikitsa kafukufuku wawo kufuna kumanga anthu omwe anayambitsa ziwawazi, ndipo pofika lero lachitatu apolisi-wa amanga anthu okwana anayi.

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here